Khristu Mu Nyimbo · Christ in Song Chichewa
154. Mlonda, Tandiuza Ine
WATCHMAN, TELL ME
WATCHMAN, TELL ME
1. Mlonda, tandiuza ine, Kunja kuli kuchako?
Zosonyeza kudza kwake, Kodi zionekadi?
Inde, mlendo, taonani, Kucha kwayandikiratu,
Vala za kukoma zako, Kuli kucha, dzuka ’we.
2. Mlonda, nyali iwunika Mommo m’njira mwakomo;
Zozizwitsa m’dziko monse, Zisonyeza tsikulo.
Podzaomba pa lipenga, Pakudzuka a ku manda,
Omwalira mwa Ambuye, Adzavala chosafa.
3. Mlonda, fu’la lili kudza Tsiku lalikululo.
Onse alalike kuti, Mfumu yayandikatu.
Inde, mlendo ’we, ndiona, Dziko lopambana lija.
Mzinda wopambana yonse, Uwoneka tsidyalo.
4. Mlonda, undiuze ine, Za mu mzinda momwemo,
Mmene Mfumu ikukhala, Pa chimpando chakecho.
Dziko lija likuwala Ndi ulemerero wake;
Kuli duwa ndi mitengo, Ndi mitsinje yoposa.
5. Dzuwa lituluka ndithu, La usana womwewo.
Onse alalike kuti, Tsiku layandikatu.
A ulendo aonenso, Kuli phiri la Mulungu;
Tidzafika konko msanga, Tidzakondwererako.
Help keep these hymns free
Your donation can help maintain the website, improve accessibility and keep the hymns freely available.
♥ DonateHymn details
Hymnal: Khristu Mu Nyimbo
Search name: Christ in Song Chichewa
Language: Chichewa
Hymn number: 154
Permanent page: number and title URL
This page preserves Mlonda, Tandiuza Ine as Hymn 154 in Khristu Mu Nyimbo. It is part of the Christ in Song Chichewa collection within a multilingual Adventist hymn archive built for reading, searching, sharing and comparing hymn traditions across languages.
Use the previous and next buttons to continue through this hymnal, or return to the collection page to search by number and title. The reading tools above let you adjust text size, save favourites and share the hymn with others.
Reading and preservation note
Historic and regional hymn texts can contain spelling differences, older punctuation, local wording and transcription variations. This archive keeps the hymns searchable while allowing future corrections and improvements to be made carefully.