Christ in Song Christ in Song Chichewa

Khristu Mu Nyimbo · Christ in Song Chichewa

249. Nkhosa Zambiri M’Kholamo

THERE WERE NINETY AND NINE

THERE WERE NINETY AND NINE

1. Nkhosa zace zambiri m’kholamo
Anasunga mbusayo
Anasunga mbusayo
Imodzi inasocerera,
Yotaika ku thengo.
Kutari ku phiri loopsya
Kutari ndi mbusa waceyo
Kutari ndi mbusa waceyo.

2. Mbuye, muli zambiri m’kholamu
Kodi sizikwanira?
Nayankha mbusa, ndi yangayo
Imene yataika.
Ngakhale njoopsya njirayo,
Ndilinga ku phiri kupeza.
Ndilinga ku phiri kupeza.

3. Koma opulumuka sadziwa
M’khwawa mbusa napyola,
Ndi mdima wo’psya usikuwo
Polonda nkhosayo.
Anamva kulira kutari
Mapeza yofo’ka, ikufa.
Mapeza yofo’ka, ikufa.

4. Mbusa, ndiona mwazi m’njirayi;
Ndi cifukwa ciani ko?
Ndinaukhetsa potsata’we,
Kubwenza ku kholako.
Ndi m’manja mwalaswa bwanjimo?
Ndalaswa pofunafuna’we.
Ndalaswa pofunafuna’ we.

5. Ndipo ponse pa phiri ndi m’dambo,
Ndi m’makwawa ponsepo
Namveka liu lopfuula,
Kondwerani ndapezayo.
Angelo a Mlungu nayankha.
Ambuye napeza nkhosayo.
Ambuye napeza nkhosayo.

Help keep these hymns free

Your donation can help maintain the website, improve accessibility and keep the hymns freely available.

Hymn details

Hymnal: Khristu Mu Nyimbo

Search name: Christ in Song Chichewa

Language: Chichewa

Hymn number: 249

Permanent page: number and title URL

This page preserves Nkhosa Zambiri M’Kholamo as Hymn 249 in Khristu Mu Nyimbo. It is part of the Christ in Song Chichewa collection within a multilingual Adventist hymn archive built for reading, searching, sharing and comparing hymn traditions across languages.

Use the previous and next buttons to continue through this hymnal, or return to the collection page to search by number and title. The reading tools above let you adjust text size, save favourites and share the hymn with others.

Reading and preservation note

Historic and regional hymn texts can contain spelling differences, older punctuation, local wording and transcription variations. This archive keeps the hymns searchable while allowing future corrections and improvements to be made carefully.