Christ in Song Christ in Song Chichewa

Khristu Mu Nyimbo · Christ in Song Chichewa

73. Pobwera Mfumu

CALLED TO THE FEAST

CALLED TO THE FEAST

1. Taitanidwatu ku phwando, Kukhala nao anthu ake;
Chidzaonekanji kwa ife, Pobwera Mfumu?

* CHORUS:
Pobwera Mfumu, mbale, Pobwera Mfumu!
Chidzaonekanji kodi, Pobwera Mfumu?
*
2. Adzavala korona Iye, Amene anafera anthu;
Tidzamuona bwino-bwino, Pobwera Mfumu.

3. Monga kung’anima kwa mphezi, Zobisika zidzaoneka
Tidzadziwana wina mnzake, Pobwera Mfumu.

4. Adzaona anthu akewo, Atavalatu zoyerazo;
Tikapirira tidzakondwa, Pobwera Mfumu.

5. Kulekana kwa nthawi zonse, Kulira kwa anthu ochimwa,
Kudzakhala koopsa ndithu, Pobwera Khristu.

6. Ambuye tilandirenitu, Tikhale pafupi nanutu,
Kuti tisadzaope konse, Pobwera Inu.

Help keep these hymns free

Your donation can help maintain the website, improve accessibility and keep the hymns freely available.

Hymn details

Hymnal: Khristu Mu Nyimbo

Search name: Christ in Song Chichewa

Language: Chichewa

Hymn number: 73

Permanent page: number and title URL

This page preserves Pobwera Mfumu as Hymn 73 in Khristu Mu Nyimbo. It is part of the Christ in Song Chichewa collection within a multilingual Adventist hymn archive built for reading, searching, sharing and comparing hymn traditions across languages.

Use the previous and next buttons to continue through this hymnal, or return to the collection page to search by number and title. The reading tools above let you adjust text size, save favourites and share the hymn with others.

Reading and preservation note

Historic and regional hymn texts can contain spelling differences, older punctuation, local wording and transcription variations. This archive keeps the hymns searchable while allowing future corrections and improvements to be made carefully.